Wolemba Joseph Kaipa
Malawi UMC Communicator
Maphuziro abusa omwe anachitikira ku ofesi yaikulu mu mzinda wa Blantyre kuyambira pa 12mpaka pa 16 september 2011 athandiza kusula ophuzirawa kukhala akadaulo pa ntchito imene Mulungu anawapatsa.
Maphunzirowo amene anakozedwa ndi cholinga chosula abusa ochuluka m’Malawi muno athandizira kuti mpingo wa United Methodist upite chitsogolo ndi utumiki wake. M’modzi wa ophunzira pa maphunzirowo, Obed Ngulube kuchokera ku seketi ya Livingstonia wati wapindula kwambiri ndi maphunzirowa . Iye anati akakhunthulira nthumba la chidziwitsoli kwa athu ochuluka mu seketi yake pokhala chitsanzo pa zomwe aphunzira potero anthu adzakhala omvetsetsa ndi okozeka kulandira zosowa zawo za moyo wauzimu.
M’mawu ake m’busa Steve Mbewe yemwe adali mgulu lophunzitsa abusawa, anati ali wokondwa kwambiri ndi m’mene maphunzirowa anayendera. Iye anati ophunzira amamvetsera bwino, kufunsa pamene sanamvetsetse komanso kuwerenga mwakathithi kukonzekera mayeso amene analemba pamapeto a maphunzirowo. Mbewe anatinso pali chiyembekezo kuti abusawa akayamba kuphunzitsa ana awo ndi ena mu mpingo kuti adzakhale mzika zodalirika mu m’mpingo wa United Methodist kuno ku malawi.
Mkulu wa mpingowu ku Malawi m’busa Daniel Mhone anathirirapo ndemanga kuti maphunzirowo akhala opambana chifukwa cha kudzipereka komanso kudalira pemphero kwa ophunzirawo pamodzi ndi komiti yomwe inakonza. Iye anati ngankhale panali mayesero osiyanasiyana monga matenda ndi ena omwe mdyerekezi anayesetsa kuvumbwitsa mmasikuwa, Mulungu anamenya nkhondo pochiritsa ndi kukhalitsa bata ziwanda zonse zofuna kusokoneza mpaka maphunziro anatha m’nthawi yake. Mhone anapitiriza kuti maphunzirowa athandizanso kuti abusa omwe angosankhidwa kumene ndi Bishop kupita m’maseketi akhale ndi poyambira pa utumiki wawo.
Pomaliza Mhone anauza abusa onse kuti kuikidwa kapena kupatsidwa seketi yotumikira sizikusonyeza kuti payikidwa malire kwa abusa kukatumikira seketi ina.Iwo anati abusa akhoza kuyenderana m’maseketi ngati alumikizana mokwanira komanso kudziwitsa ofesi yawo ndipo anaonjezera kuti kuyenderana kwa abusa m’maseketi kumalimbikisa ubale pa ntchito ya utumiki mu mpingo.
M’busa Teddy Crum yemwe ndi m’mishonale kuno ku Malawi komanso amaphunzitsa abusawo, anathirira ndemanga kuti mpingo wa United Methodist umankhazikika kwambiri pa kuphunzitsa atsogolereri kuti adziwiretu chochita m’mene akukayamba ntchito yawo. Iwo anapereka chitsanzo cha abusa omwe angosankhidwa kumene ndi Bishop kuti panopa akudziwa m’mene angagwilire ntchito yawo. Crum anapitiriza kuti maphunzirowa athandiza abusawa kumanga maziko autumiki komanso kukhala ozidalira ndipo anatinso anthu ayenera kusiyanitsa kumbali ya utumiki. Anaonjezera kuti pali utumiki wina ongosakhidwa ndi anthu pamene wina umankhala maitanidwe kuchokera kwa Mulungu. Pophera mphongo pa mfundoyi iye anati ena amangosakhidwa chifukwa choti amapezeka mu zochitika monga:makwaya,kulalika ndi kutsogolera chipembedzo koma akasankhidwa kuti akatumikire m’dera lina sachita zimene aphunzira ndi zimene mzimu afuna. Pamene iwo amene ali osankhidwa amachita zimene aphunzira mogwirizana ndi zimene mzimu ukufuna. Posonyeza kuikapo mtima pa utumiki womwe Mulungu anamuninkha mtumikiyu wayendera maseketi asanu ndi awiri omwe maina ake ndi Kamwendo, Mulanje, Mpenya, Madisi, Bethel, Mzuzu ndi Nsanje ndipo anati ali wokondwa poona kuti abusa ochuluka akugwiritsa ntchito zimene anaphunzirazo. Iye anati izi zithadiza kuti zinthu zisithe m’maseketi ochuluka m’malawi muno ndipo anatsindika kuti apitiriza kuyendera maseketi omwe atsara mogwirizana ndi abusa akuluakulu a mpingo m’malawi muno kuti aone m’mene ntchito ya ambuye ikuyendera.
No comments:
Post a Comment